AMUPHERANJI CHILIMA ? IMFA YOWAWA YA SAULOS CHILIMA

Поделиться
HTML-код
  • Опубликовано: 11 июн 2024
  • A CHILIMA AMWALIRA PA NGOZI YA NDEGE
    Dziko la Malawi lili pa chisoni chachikulu pamene nzika zake zikulira kwambiri kamba ka ngozi ya ndege imene yatenga miyoyo ya anthu asanu ndi anayi (9) amene ndikuphatikizapo wachiwiri wa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Klaus Chilima. Ndegeyi imene inanyamula anthuwa inagwa dzulo pa 10 June 2024 ku dera lotchedwa Nthungwa mu nkhalango ya Chikangawa m’boma la Mzimba. Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ndi amene alengeza ndikuwuza mtundu wa a Malawi pazakumwalira kwa a Chilima ndi anthu ena amene anali nawo mu ndegeyo masana alero pa 11 June 2024. Mukuyankhula kwawo, a Chakwera amene amanveka ndikuwoneka kuti ali ndi chisoni chachikulu, apempha anthu mdziko muno akhale pa umodzi a bata pa nthawi yovuta ngati imeneyi.
    A Chilima amapita ku Mzuzu kuchoka ku Lilongwe komwe amati akapitilira kupita m’boma la Nkhatabay kumene amayenera kukakhala nawo pa mwambo woyika mmanda a Ralph Kasambara amene anamwalira ku mapeto kwa sabatayi. Komatu za chisoni, nyengo ya chifunga inakakamiza ndege ya asilikali ankhondo adziko lino kuti ibwelere ku Lilongwe itakanika kutera pa bwalo la Mzuzu ndipo kuchoka apo, akulu akulu owona za ma ulendo a pandege ku Mzuzu ko sanathenso kuyankhula nayo ndegeyo.

Комментарии • 51

  • @mara88i
    @mara88i Месяц назад +2

    To be aware is to be alive #MCP poly tricks #assassinations #RIP #vicePRESIDENT #saulosCHILIMA

  • @spartalemani4389
    @spartalemani4389 Месяц назад +1

    We here bro

  • @user-lj7lm6ly7z
    @user-lj7lm6ly7z Месяц назад +4

    Mutu wa nkhaniwo ndizonwe mukuforokozazo zikusephana,and zoti achita kumupha ife tazidziwa kale through Limpopo FM Inu mwatsalira pati

    • @RodgersPhiri-ju1eo
      @RodgersPhiri-ju1eo Месяц назад

      Ilinde boza lenileni kodi amayendesa ndege anali chakwela koma munyasa anakonza nde chabwino poti inu mukuziwabwino mulindiumboni bwanji mutithandize mupite kupolisi mukawafotokozele venvenve wankhaniyi kuti amene apanga izizi amangidwe chifukwa or atakhala president amamangidwa bola umboniwanuwo please tithandizeni chilungamo chilibe mantha

    • @DorrahBanda
      @DorrahBanda Месяц назад

      Ndipo inu mmmm

  • @HalisonSolomon
    @HalisonSolomon Месяц назад +1

    Nkhani ndiyoti mcp yampha anthu 8 + vice president saulos chirima,enanu mutsutse musatsutse izi ndizomwe a Malawi akudziwa,CHIFUKWA ngozi ikachitika anthu ma foni amapezeka kena kotchedwa black box kamayenera kupezeka koma apo kanazulidwa anazula ndani konseko kufuna kubisa umboni kutenga ma phone a anthu akufao kufuna kubisa umboni, MCP boma lakupha lapha tsogolo la amalawi,musaikire KUMBUYO mimbulu

  • @harrisbanda5891
    @harrisbanda5891 Месяц назад

    Awaaaaa

  • @user-ey6in8is5h
    @user-ey6in8is5h Месяц назад

    Hello Hanifa TV kodi simungapeze wina olankhura bho bho, kuti adzitipatsira uthenga?

  • @HastingsChilima
    @HastingsChilima Месяц назад +1

    Ine nnatchela nkhutu kuti ndimva zogwirizana ndi mutu wankhani koma ai palibe chikumvekapo apa mmmm

  • @mussahowen1372
    @mussahowen1372 Месяц назад +1

    Nchifukwa adawa anthu ayamba kuwasiya chifukwa mutu wakhani ndi khani zimasiyana

  • @giftdulamkalenga7344
    @giftdulamkalenga7344 Месяц назад +1

    Linthumbu ndi lomwe lamupha mkulu uyu NDIGWESE APM WAZIGWESA YEKHA LERO

  • @Geraldmkwewu
    @Geraldmkwewu Месяц назад

    Kod lnuso mkularata chani voice yosamveka fundo apa nkhani ndiyoti mcp yatipha lfe amalawi achinyamata 😭😭ngt boza chilima wanthu wk lmozi kumpha anthu 10 osalakwa chilima Ralph ndi nonse akupherani kumoz kawuseni mtendere tilibe mawu zawo zayera

  • @user-co3wr3rn4h
    @user-co3wr3rn4h Месяц назад

    Nkhani tayiwona, kale ife mcp yapha chilima ndipo simuzawonaso vote inu a galu

  • @chikublea8982
    @chikublea8982 Месяц назад +2

    Inuyo simumatha

  • @Extratremendouszeus
    @Extratremendouszeus Месяц назад

    Ndiwe mbuzi
    Ungonena zamisala ...ndipo usamalankhule ngat ukuvina

  • @RodgersPhiri-ju1eo
    @RodgersPhiri-ju1eo Месяц назад

    Ine ndimadabwa kwambiri kwathu kuno kumalawi kaya ndimaganizo awumphawi kaya umbuli anthu tikuchita kuwona kuti anthu amwalila pangozi koma umunva wina ati mwamuphelangi m'mbale wathu nde funso kumati wamupha ndani oyendesa ndegeyo kapena ndani nanga woyendesayo kapena kuti amene anakwelanawo ndegeyo anayikonda infayo kuti amwalile zina tikamayankhula tizikhala ndiwumunthu oyendesa sangalole kuti agwese ndege aphe achilima poziwa kuti naye amwalila osatheka ndani safuna moyo

  • @TelBit-hm4fb
    @TelBit-hm4fb Месяц назад +1

    Kodi black box ili kuti ya ndegeyo
    Ndi imene ingathandize kuuza anthufe amene tikulephera kupeza mayankho eni eni chifukwa zomwe tikuuzidwa sidzikumveka bwino

    • @joyedward45
      @joyedward45 Месяц назад

      I don't think atayipeza anga bwere poyera mmmm ,koma kuona zinthu za a chilima mmm abale koma dziko munthu ndi oopsa shame kodi ndegeyo imayendera madzi or mphepo mmmm munthu wandiopsa hey

  • @KunyengaMoyo
    @KunyengaMoyo Месяц назад +1

    Wachita kuphedwa kodi???

  • @AbudulRaheembakaliwillard
    @AbudulRaheembakaliwillard Месяц назад +1

    Rip

  • @JohnAsendi
    @JohnAsendi Месяц назад

    Basi anyama yayikuluwo akhale vp si apenze mtima agalu chabe chabe apa ndiye mwazinyera mkabudula ndiye mudzawina bwa popanda n'gwilizano poti mudawinila those zipani npaka 30 kulimbana ndi chipani chimozi Hedeee tidzaonesana 2025 bola otsazi Inshaallah 😁😁😁😁😁

  • @jamesjolichi2026
    @jamesjolichi2026 Месяц назад

    😢😢😢😢

  • @SamuerYohane
    @SamuerYohane Месяц назад

    😢😢😢

  • @gesinasutherland9241
    @gesinasutherland9241 Месяц назад +1

    Well done Hanifa..nkhani yopatsa chidwi..koma mutu wankhaniwutu mwalakwitsa..Mzimu wa vote yanga upitilize kuwunsa mu mtendere..😢😢

  • @JimmyIsaac-xd4ef
    @JimmyIsaac-xd4ef Месяц назад

    Chakwera ndiye wapha anthuwa Ife tamva kale. Inu munalikuti

  • @user-fm1vj8ty9d
    @user-fm1vj8ty9d Месяц назад

    Awa nawonso kungotichedwesapo apa mutu wankhani ndizimene akuyankhula tsizikugwiridzana

  • @MathewsLongwe-ix8ps
    @MathewsLongwe-ix8ps Месяц назад

    Fotseki😢😢😮

  • @NgomaRaheem
    @NgomaRaheem Месяц назад

    Mutu ndi nkhani zizifananako pls

  • @paulnyondo7572
    @paulnyondo7572 Месяц назад

    Tikufuna bakili muluzi tv yiyankhulepo

  • @quitsa3463
    @quitsa3463 Месяц назад

    Ndiwe mbuzi title ndi nkhani zikusiana

  • @AlinafeKumanda
    @AlinafeKumanda Месяц назад

    Zimu wachima uuse muntendere

  • @JamihFernandoSimao
    @JamihFernandoSimao Месяц назад

    Awaso nde achitsilu kwambili bwanj
    Nthawi inoyo ungamasemphanitse mutu wankhani?
    Simutha ndinu opepela kwambili

  • @nickgunda8778
    @nickgunda8778 Месяц назад +1

    Voice yanuyo simveka bwino mupeze wina azikuyankhulilani

  • @harrisbanda5891
    @harrisbanda5891 Месяц назад

    Zaziiiiii

  • @unarinematshomo2841
    @unarinematshomo2841 Месяц назад

    Mutu wa nkhani, utiuza zina inuso ndeee tive ziti??????

  • @harrisbanda5891
    @harrisbanda5891 Месяц назад

    Awaaaaanso mmene amawelengela nkhani zawoo , eish,

  • @YasinMusa-ym8lp
    @YasinMusa-ym8lp Месяц назад +1

    😂😂😂😂

  • @hopeskafumbiphiri6011
    @hopeskafumbiphiri6011 Месяц назад +2

    i dont like the way you read eish its boring

  • @DanMhone-iw6xg
    @DanMhone-iw6xg Месяц назад

    Zachamba palibe chomwe ndva zazi kunena mokakamizidwa kuti unene ngat voice yako sikuwoneka ngati osamatiyamba dala zopusa

  • @user-zl9vj6hc6y
    @user-zl9vj6hc6y Месяц назад

    Mutu wa nkhani ukupita Ku Blantyre zimene mukufotokonza zikupita Ku Zomba.... Yankhulani Ngati mnyamata.... Title and story must be the same... Come on man!!!!

  • @YusufuUsumani
    @YusufuUsumani Месяц назад

    Kodi iwe yangulani mutu wankhani

  • @user-kj9bu2xc5t
    @user-kj9bu2xc5t Месяц назад +1

    Uyu ndiwamatha kwambiri is not a freedom fighter that'swhy Bakili Muluzi TV is a best ever. Most of his story mmmm 2/10

  • @user-xb2wm1zi4p
    @user-xb2wm1zi4p Месяц назад

    Apa ndi amupheranji? Kapena mbiri yake?

  • @harrisbanda5891
    @harrisbanda5891 Месяц назад

    Hanifa utube ithe, siimatha kulondoloza nkhani komanso ili ndi anthu osatha kuwelenga bwino nkhani kkkkkkkkkkk, makamaka uyu akuwelenga panoyu akungowelenga ngati bembelezi kkkkkkkkkkk

  • @jesterkalumba2660
    @jesterkalumba2660 Месяц назад

    Rubbish video u R talking of useless things instead of tackling the heading...wa bakili muluzi uja ndi dolo osati iwe kutiuza za obvious

  • @JonathanSymon
    @JonathanSymon Месяц назад

    😂😂😂😂