ZIFUKWA ZIMENE BON KALINDO WAMANGIDWA KAWIRI MU TSIKU LIMODZI

Поделиться
HTML-код
  • Опубликовано: 8 сен 2024
  • Lachiwiri, pa 2 April 2024, apolisi mu mzinda wa Lilongwe anamanga mkulu ochita zitsuzo, wandale komanso amene pano amamenyera ufulu wa anthu a Bon Kalindo ati kamba kowaganizira kuti anapanga ndikutsindikiza uthenga wina pa makina a internet umene ukhoza kubweretsa chisokonezo ndikusokoneza chitetezo mdziko muno. lachinayi pa 4 April 2024, a Kalindo anakawonkera ku bwalo la milandu la Lilongwe Magistrate kumene boma limawauza zifukwa zenizeni zomwe awamangira ndipo iwo amakapempha belo. Galimoto ya polisi imene inawanyamula a Kalindo itafika, iwo anatuluka mwamsangala uku atakweza manja awo mmwamba kuwonetsa ku gulu la anthu unyolo umene apolisi anawamanga. Pamene amafika kumeneku nkuti a Kalindowa atavala ovololo yofiira imene chapa mtima pake panalembedwa mawu akulu akulu akuti BEK chimene ndi chidule cha dzina lawo lonse la Bon Elias Kalindo. Iwo nkutinso mmutu mwawo anali atamanga zingongo zimene zabwera pamene akhala akusunga tsitsi lawo kwa nthawi yayitali.

Комментарии • 28