LACHINAI LA MULUNGU WA 7 WA PASAKA/16 MAY 2024/ FR FRANCIS DAMASEKE DP

Поделиться
HTML-код
  • Опубликовано: 14 май 2024
  • TIYANKHULENI AMBUYE
    16 MAY, 2024
    LACHINAI LA MULUNGU WA 7 WA PASAKA
    kulemekeza Ubaldus Woyera
    MAU OYAMBA A MBUKU LA NTCHITO ZA ATUMWI 22:30,23:6-11
    _Limba mtima. Monga wandichitira umboni kuno ku Yerusalemu, uyenera kukandichitiranso umboni ku Roma_.
    Mkulu wa asirikali uja adafuna kudziŵa kwenikweni chifukwa chimene Ayuda adadzanenezera Paulo. Choncho m’maŵa mwake adammasula, nalamula kuti akulu a ansembe ndi onse apa Bwalo Lalikulu la milandu la Ayuda asonkhane. Kenaka adabwera ndi Paulo namuimika pakati pawo. Pamene Paulo adaona kuti ena mwa iwo ndi a m’gulu la Asaduki, ena a m’gulu la Afarisi, adanena mokweza mawu m’Bwalo muja kuti: “Abale anga, inetu ndine Mfarisi, mwana wa Mfarisi. Ineyo ndikuweruzidwa chifukwa ndimakhulupirira kuti anthu adzauka kwa akufa.” Atanena zimenezi, Afarisi ndi Asaduki aja adayamba kukangana, ndipo msonkhano udagaŵana. Paja Asaduki amati anthu sadzauka kwa akufa, ndiponso kuti kulibe anjelo kapena mizimu. Koma Afarisi amakhulupirira zonsezi. Anthu aja adayamba kufuula kwambiri. Tsono aphunzitsi ena a Malamulo, a m’gulu la Afarisi, adaimirira nanenetsa kuti: “Sitikupeza konse cholakwa mwa munthuyu ayi. Mwina nkukhala kuti mzimu kapena mnjelo walankhula naye!” Anthu aja adafika pokangana koopsa, kotero kuti mkulu wa asirikali uja ankaopa kuti angamkhadzule Paulo. Choncho adalamula asirikali kuti: “Pitani mukamlanditse kwa anthuwo, mukamloŵetse mu linga la asirikali.” Tsiku lomwelo, usiku, Ambuye adadzaima pafupi ndi Paulo namuuza kuti: “Limba mtima. Monga wandichitira umboni kuno ku Yerusalemu, uyenera kukandichitiranso umboni ku Roma.”
    Mau a Ambuye
    NYIMBO YA SALIMO: SALIMO 16: 1-2A, 5, 7-8, 9-10, 11
    Mundisunge, Inu Mulungu, pakuti Ndinu kothaŵira kwanga (1).
    Mundisunge Inu Mulungu, pakuti ndikuthaŵira kwa Inu.
    Ndimamuuza Chauta kuti: “Inu ndinu Ambuye anga.”
    Chauta ndiye chuma changa ndi choloŵa changa.
    Tsogolo langa liri m’manja mwanu.
    *Mundisunge, Inu Mulungu, pakuti Ndinu kothaŵira kwanga*.
    Ndikutamanda Chauta amene ali phungu wanga.
    Mtima wanga umandilangiza ndi usiku womwe.
    Nthaŵi zonse ndimalingalira za Chauta.
    Popeza kuti ali ku dzanja langa lamanja,
    Palibe amene angandiopse konse.
    *Mundisunge, Inu Mulungu, pakuti Ndinu kothaŵira kwanga*.
    Nchifukwa chake mtima wanga ukukondwa,
    Ndipo mkatikati mwangamu ndikusangalala.
    Thupi langanso lidzakhala pabwino,
    Chifukwa simudzandisiya ku malo a anthu akufa,
    Simudzalola kuti wokondedwa wanune ndikaole kumeneko.
    *Mundisunge, Inu Mulungu, pakuti Ndinu kothaŵira kwanga*.
    Mumandionetsa njira ya ku moyo.
    Ndimapeza chimwemwe chachikulu kumene kuli Inu,
    Ndidzasangalala mpaka muyaya ku dzanja lanu lamanja.
    *Mundisunge, Inu Mulungu, pakuti Ndinu kothaŵira kwanga*.
    *Aleluya*: (Yohane 17: 21) Ndikuŵapempherera kuti iwo onse akhale amodzi. Monga Inu Atate mumakhala mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, iwonso akhale mwa Ife. Motero anthu onse adzakhulupirira kuti mudandituma, *Aleluya*.
    MTHENGA WABWINO MONGA ADALEMBERA YOHANE 17:20-26
    _Ndikuŵapempherera kuti iwo onse akhale amodzi_.
    Yesu adakweza maso Kumwamba napemphera kuti: “Sindikupempherera iwo okhaŵa ayi, komanso amene adzandikhulupirira chifukwa cha mawu awo. Ndikuŵapempherera kuti iwo onse akhale amodzi. Monga Inu Atate mumakhala mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, iwonso akhale mwa Ife. Motero anthu onse adzakhulupirira kuti mudandituma. Ulemerero womwewo umene mudandipatsa, ndaŵapatsanso iwoŵa. Akhale amodzi monga Ife tili amodzi. Ine ndikhale mwa iwo, Inu mwa Ine, kuti akhale amodzi kwenikweni. Motero anthu onse adzazindikira kuti mudandituma ndinu, ndipo kuti mumaŵakonda monga momwe mumandikondera Ine. Atate, ndifuna kuti amene mudandipatsa, iwonso akhale pamodzi ndi Ine kumene ndili. Ndifuna kuti aone ulemerero wanga umene mudandipatsa, chifukwa mudandikonda dziko lapansi lisadalengedwe. Atate olungama, anthu ongokonda za pansi pano sadakudziŵeni ayi, koma Ine ndimakudziŵani, ndipo aŵa ali panoŵa akudziŵa kuti ndinu mudandituma. Ndidaŵadziŵitsa dzina lanu, ndipo ndidzaŵaphunzitsabe. Ndifuna kuti chikondi chimene mumandikonda nacho, chikhalenso mwa iwo, ndipo Ine mwa iwo.”
    Mthenga wa Ambuye

Комментарии • 9